Patadutsa nthawi yayitali pakumveka mphekesera zoti chipani cha Democratic Progressive (DPP) chagula ndege pokonzekera kampeni yamasankho omwe achitike chaka chamawa, chipanichi kudzera mwa m’neneri wake bambo Nicholas Dausi chafika poyera tsopano kutsimikiza zankhaniyi.

Malingana ndi bambo Dausi, chipani chawo cha DPP tsopano chamaliza kuchita dongosolo lonse loti ndegezi zomwe ndi ziwiri zamtundu wa ‘helicoptor’ zibwere m’dziko muno.

Bambo Dausi ati, DPP inagula kale ndegezi ndipo chomwe chatsala ndichakuti zibwere m’dziko muno koma iwo akana kunena tsiku lenileni lomwe ndegezi zitere panthaka ya Malawi.

You May Also Like

16 NDEMANGA

  1. K61bn kwabwela ziwiri basi ndikuti K61bn siinathe koma chimenecho ndichitukuko cha ndani? mukuona ngati dziko lanthu likusaukila magalimoto ammwambao

  2. malo moti ndalama zimenezo zithandizire anthu mesa imeneyo nde campaign yabwino mukuona ngati ife tidzavotera apetulowo kamba koti akutsika mundege aaaah mbava ndimadabwa dausiyu nkhope imachita kuoneka madzi madzi ngati galasi kuli kudya ndalama zathu aaah pano nkhope ikuoneka ngati amadzola ambishubaba

ZIMENE MUMAKONDA

Please enter your comment!
Please enter your name here

From The World