President Peter Mutharika wasankha Justice Jane Ansah kukhala wapampando wa bungwe lazachisankho la Malawi Electoral Commission (MEC).

Ansah walowa m’malo mwa malemu Maxon Mbendera omwe anamwalira mwezi watha atangogwa pa mpando ku Lilongwe akugwila nchito zina zokhuza ofesi yake.

Mlembi wamkulu wa boma a George Mkondiwa ati kusankhudwaku kukuyambila lero.

Justice Ansah anali judge ku bwalo la apilo.

You May Also Like

ZIMENE MUMAKONDA

Please enter your comment!
Please enter your name here

From The World