Mzibambo wazaka makumi atatu ndi zitatu (33) wagamulidwa kuti akakhale kundende miyezi makumi anayi ndi ziwiri (42) kamba kopezeka olakwa pa mlandu opanga zadama ndi mamuna mzake.

Oyimira apolisi pa nkhaniyi, Patrick Chipote anauza khothi kuti a Stanley Chiponda adapalamula mlanduwu pa 2 januwale 2018 pa Msika wa Nambuma ku Dowa.

Malingana ndi a Chipote, a Chiponda adanyengelera ndi mowa Mnyamata wa zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri (17) pa tsikulo. Ali mkati mokumwa mowa, Bamboyu adakokera mnyamatayo munyumba ina yosamaliza komwe adachita zadamazo.

Nkhaniyi idakasiidwa m’manja mwa amfumu mderalo omwe adakaipereka ku police yaing’ono ya Nambuma.

Ku bwalo la milandu, a Chiponda adapempha bwalolo kuti liwapase chilango chofewerako malingana ndikuti ndi okwatira komaso ali ndi udindo wa ukulu ku banja lawo.

Koma a Chipote adawuza bwalo kuti M’bamboyu akuyenera kupatsidwa chilango chachikulu malingana ndikuti ngakhale adali atamwa mowa, zidawonetsa kuti zonsezi zidali zochita kukonza.

Adapitiriza kunena kuti nkhaniyi yasokoneza kakhozedwe ka mkalasi ka myamata wa zaka zachichepereyo.

Popereka chigamulo, a Yohane Nkhata a bwalo la milandu la Mponera adagwirizana ndizomwe adanena a Chipote ndipo adalamula a Chaponda kuti akakhale kundende kwa miyezi makumi inayi ndi ziwiri pofuna kuti ena atengerepo phunziro.

A Chaponda amachokera m’mudzi wa Tuzwire Mdera ya mfuma yaikulu Kayembe ku Dowa.

You May Also Like

ZIMENE MUMAKONDA

Please enter your comment!
Please enter your name here

From The World