Gulu lina la anthu lapempha Dr Saulos Chilima kuti achotse mamembala ena omwe ali mu United Transformation Party (UTM) ati kamba koti ali ndi milandu yomwe yosiyanasiyana.

achilima apemphedwa kuthothola anthu ena mu UTM

Mu kalata yomwe anthuwa alemba, iwo ati mamembala ena akulu akulu a UTM asiye kumauza anthu kuti ali mu mgwirizanowo pokhapokha milandu yawo italowa mu bwalo la milandu.

Anthuwa ati ena mwa mamembalawo ndi a Patricia Kaliati, Noel Masangwi, Ralph Kasambara, Richard Makondi komaso a Louis Ngalande.

“Ngakhale kuti UTM yapereka chikoka kwa anthu, koma ife taganiza kuti tikupempheni mtsogoleri wathu kuthothola ena mwa mamembalawa kuti zomwe tiziauza amalawi zizikhaladi zoona zenizeni ndiposo zomwe zidzachitike tikatenga boma mu 2019.

“Titsimikize kuti membala aliyense mu UTM Sali okhuzidwa ndi zakatangale zilizonse kuti zipani zina zisowe pothawira zikafuna kukamba zoipa za UTM, “iwo atero.

Achilima akhazikitsa mgwirizano wawo wa UTM kuchigawo cha kum’mwera lamulungu langothari ku Njamba Freedom Park komwe kunasonkhana chinantindi cha anthu.

 

You May Also Like

ZIMENE MUMAKONDA

Please enter your comment!
Please enter your name here

From The World