Katswiri oyimba chamba cha reggae Angola Maseko akubwera m’dziko la Malawi m’mwezi wa August, 2018 kudzaonetsa zisudzo zake ku Robin’s park ku Zomba pa mwambo wa Rastafari wokwanitsa zaka makumi asanu ndi zitatu (53) amfumu Haile Selassie pamene anabwera kuno ku Malawi.

Maseko azakhala m’modzi wa anthu akulu akulu pa mwambo wauzimu pangodya la phiri la Zomba. Mayimbidwe azakhala molondolozedwa ndi Jah B waku zambia, Ma Blacks ndi Lucius Banda.

M’chaka chino, mwambowu ukhala ukuchitika kwa masiku awiri. Malingana ndi omwe akonza mwambowu, kuzakhala mapemphero kuyambira pa 4 August m’mawa mpaka pa 5 August. Mwambowu udzayambira ku Emperor’s View ndipo ukathera ku Gynkana Club pa 5 August madzulo ake.

Maseko watsimikiza kudzakhala nawo pa mwambowu kudzera pa kachidutswa ka kanema komwe ka kuzungulira pa tsamba la facebook komanso pa WhatsApp.

 

You May Also Like

ZIMENE MUMAKONDA

Please enter your comment!
Please enter your name here

From The World