Friday, April 26, 2024

Featured Video

Latest Stories

Top 10 Music

Upcoming Events

Zomba City Festival

Fri, 26 Apr 2024 10:00:00 UTC @ Botanic Garden - 2024 Zomba City Festival is schedulled to take place on 26 to 28 April at Botanic Garden in Zomba This is a festival for all ages in the historic mountain city of Zomba. Celebrate Cultu... More Info
Queens Club Shut Down

Fri, 26 Apr 2024 19:00:00 UTC @ Queens Club - Queens Club Presents "Queens Club Shut Down" with music performances by Kelly Kay, Charisma, Teddy Makadi and Praise Umali. The show will take place at Queens Club in Mzuzu on 26 April... More Info

Apolisi Anjata Dotolo Wa Chinyengo Ku Ntchisi

Doloto wachinyengo Clifford Chimtengo anapeleka mankhwala osakhalabwino kwa anthu anayi m’mudzi wa Joshua m’boma la Ntchisi.

Elise Kapolo (kumam’zere) ndi amuna awo bambo Bizaliele.

Dotoloyo anawanamiza anthu am’mudziwo kuti iye ndi dotolo ndipo amagwira ntchito ku chipata cha Queens mum’zinda wa Blantyre.

kenako dotoloyu anapereka mankhwala kwa anthu anayi ndipo patapita ma ola angapo anthu anayiwa anadwala mwakayaka. Athuwa anawatengela ku chipatala cha Ntchisi chomwe chili kutali ndi mudziwo.

Izi zizanachitika pakati pa usiku ndipo atafika nawo anthuwa kuchipatala, Liviness Kapolo wazaka makumi asanu ndi atatu ndi chimodzi (81) anali atamwalira. Livinesi wasiya zidzukulo zisanu ndi zinayi zomwe amaziyang’ala.

Anthu atatu ena , Bizaliele Kapola mlongo wa Liviness ndi mkazi wa Bizaliele, Elise Kapolo ndi Yohane Chipokosa akupezako bwino ndipo akulandila mankwala pachipatalapo.

“Linali tsiku langa loyamba kuona munthuyo m’mudzi mwathu koma anthu ena amati adamuonapo ndipo m’kachiwiri kumuona”  Elise adafotokoza motero.

” Iye adatiuza kuti ndi dokotala am’kagwira ntchito ku Queens ndipo amakhala m’mudzi oyandikila ko Khuwi” Elise adaonjera mawu.

Pakadali Pano apolisi  anjata Clifford Chimtengo, Dotolo wachinyengoyo ndipo ali muchitolokosi kudikila m’landu wakupha munthu.

Subscribe to our Youtube Channel:

Related Posts

Face of Malawi
Face of Malawihttps://www.faceofmalawi.com
For more Info: info@faceofmalawi.com

LEAVE A REPLY

Please enter your comment!
Please enter your name here

Popular Articles