Apolisi m’boma la Dowa akusaka zimbalangondo zosadziwika zomwe zapha gogo wachizimayi wa zaka 94 zakubadwa m’mudzi mwa Chilomba, mfumu yaikulu Msakambewa.

Malingana ndi M’neneri wa polisi Sergeant Richard Mwakayoka Kaponda, adanena kuti malemuwa dzinalawo ndi Mai Talius Kwenda omwe adawapeza ataphedwa mudimba pa malo wena m’mudzi mwa Chilomba.

Powonjezera Akaponda adauza mtolankhani wathu kuti Mayi Kwenda amakhala m’mudzi mwa Chibanzi ndipo amakhala ndi chidzukulu chawo.

”Mayiwa adachoka pa khomo pawo pa 19 july,2018 m’kupita ku Lisongwe komwe kunali sadaka koma Mayiwa sadakafika kumaloko kenako ndi pamene anthu anawapeza ataphedwa mu dimba la bambo Laston Chivundula pa 21 july, 2018” Kaponda adatero.

Kenako Kaponda adaonjezera kunena kuti apolisi atafika pamalopo m’kupanga chipikisheni adaona kuti mayiwa anaphedwa ndi zipangizo zokutwa kwambiri.

Pakadali pano apolisi ali kalikiliki kufufuza anthu omwe adapha mayiwa ndipo apempha anthu am’deramo kuti awatsine khutu akanva zanthu adapha Mai Kwenda.

You May Also Like

ZIMENE MUMAKONDA

Please enter your comment!
Please enter your name here

From The World