Pali kuthekera kwakulu kuti mtsogoleri wa dziko lino, Dr Peter Mutharika komaso wachiwiri wawo, Dr Saulos Chilima – azitsogoleri awiri omwe pakadali pano ali ngati mphaka ndi khoswe pa ndale atha kukumana pa 1 sepitembala ku mwambo wa a Ngoni ku Ntcheu.

Mfumu ya angoni, Inkosi ya Makosi Gomani V yaitanitsa azitsogoleri awiriwa kuti azakhale nawo pa mwambowu omwe utazachitikire m’mudzi mwa Nkolimbo, mdera la mfumu yaikulu kwataine mboma la Ntcheu.

chithuzi chakale cha atsogoleri awiriwa

Malinga ndi chikalata chochokera kwa mfumu ya angoniyi, mtsogoleri wa dziko lino waitanidwa kuzakhala mlendo olemekezeka pa mwambowu komaso a Chilima omwe aitanidwa kuzapezeka pa mwambowu monga iwoso ndi amtundu wa chingoni.

Mwambowu omwe umatchedwa Umhlangano umachitika chaka chilichonse ndi cholinga chopititsa patsogolo chikhalidwe cha mtundu wa chi Ngoni.

Chaka chino, mwambowu uyamba pa 31 mwezi uno kumalizira pa 1 sepitembala.

Malinga ndi malamulo, mtsogoleri wa dziko ndi wachiwiri wake amayembekezeka kupasana chanza pa mwambo kapena msonkhano ulionse omwe awiriwa apezeka.

A Chilima akhala akupangisa misonkhano yawo limodzi ndi gulu la ndale lawo la United Transformation Movement (UTM) atatuluka chipani cholamula cha Democratic Progressive Party (DPP) chomwe mtsogoleri wake ndi a Mutharika.

Chitulukireni a Chilima mu DPP, azitsogoleri awiriwa akhala asakuonana ndi diso labwino monga m’mene zimakhalira khoswe ndi mphaka.

 

You May Also Like

ZIMENE MUMAKONDA

Please enter your comment!
Please enter your name here

From The World