Mtsogoleri wa dziko lino, Peter Mutharika wanenetsa kuti chipani chotsutsa cha Malawi Congress Party (MCP) sichidzalamuliraso dziko lino iye adakali moyo.

a Mutharika anenetsa kuti a Chakwera ndi chipani chawo cha MCP sichidzalamulira Malawi iwo ali moyo

Poyankhula lachinayi pa wailesi youlutsira mawu ya boma ya MBC, a Mutharika ati chipani cha MCP chomwe mtsogoleri wake ndi Dr Lazarus Chakwera sichidzaununkhaso utsogoleri wa dziko lino ati poti ndi chipani cha anthu okupha.

“Pokhapokha ngati Mutharika ali moyo, sindidzaalora amene aja kuti atenge ulamuliro wa dziko lino kachiwiri. Chimene chija ndi chipani cha anthu okupha choncho sindingaalore kudzapambana pa zisankho zikudzazi, “atero a Mutharika.

Pakadali pano, chipani cha MCP sichinayankhulepo kanthu pa mawu amene a Muntharika ayankhulawa.

Malinga ndi kafukufuku, zikuonetsa kuti chipani chotsutsa cha MCP chayamba kuposedwa mphamvu ndi  United Transform Movement (UTM) yomwe mtsogoleri wake ndi Dr Saulos Chilima.

Poyankhula za UTM, a Mutharika ati  a Chilima azinzawo ku UTM akumapanga misonkhano ndi cholinga chongofuna kunyoza atsogoleri aakuluakulu ku chipani cholamula cha Democratic Progressive Party (DPP).

You May Also Like

ZIMENE MUMAKONDA

Please enter your comment!
Please enter your name here

From The World