Pofuna kuophyeza olimbirana naye malo, mkulu wazaka 49 m’boma la Mchinji wayenda buno bwamuswe, malichoncho, chibadwile ndikuika mitumbira iwiri pa malo okanganilanawo.

Mkuluyi ali mkati mothamanga bwamuswe, Maria Jere wa zaka 52 anakatula nkhaniyi ku polisi ndipo anthu ammudzi adaona a Pontino Mbewe akuzungulira mmudzimo maliseche dzuwa likuswa mtengo.

M’neneri wa Polisi Kaitano Lubrino wanena kuti izi zachitika sabata lomwerino la chiwiri, ndipo mkuluyi adali mbulanda kwina akuimba nyimbo zopembedza mizimu.

Mkuluyi ananjatidwa ndi apolisi  tsiku lomwero, a polisi atamufusa chomwe adapangila izi, iye adati adapanga izi pongofuna kuwophyeza munthu yemwe amalimbirana naye malo komaso anthu ammudzimo.

Pontino Mbewe amachokera mmudzi mwa Tsumbs T/A Mlonyeni ku Mchinji. Mkuluyi akaima pa khothi posachedwa ndipo akayankha mlandu omwe uli otsutsana ndi section 181 and 182 mu penal code.

You May Also Like

ZIMENE MUMAKONDA

Please enter your comment!
Please enter your name here

From The World