Nyamata wazaka 18 yemwe amadziwika ndi dzina la Patrick Salimu wamwalira ku Mulanje kamba ka ndewu yomwe inabuka chifukwa cha nyama yomwe inaphedwa pa msonkhano wa chipembezo cha chisilamu wa Eid-Al-Adha.

M’bale wa omwalirayu, Sitolo Mathewe anauza apolisi kuti lachitatu lapitali, Patrick anapita ku Msonkhano wa Eid komwe anakapatsidwa nyama yoti akadyere pakhomo.

Malinga ndi m’neneri wa apolisi ku Mulanje, Greshiam Ngwira, Patrick atafika ndi nyamayo kunyumba, munthu wina anaonetsa chidwi chofuna kugula nyamayo koma malemuwa anakaniza kupanga malonda ndi munthuyo.

Mwadzidzi, munthuyo yemwe dzina lake ndi Steve Kathala anasomphola nyamayo ndi kutulutsa K200 yomwe anpereka kwa malemuwa ngati malipiro pa nyamayo, koma posakhalitsa ndewu inabuka pakati pa awiriwa.

“Pomaliza pa ndewu malemuwa anapwetekedwa kwambiri moti anthu akufuna kwabwino anawatengere ku chipatala chachikulu m’bomali komwe adamwalira mwadzidzi akufika kumene.,”adatero a Ngwira.

Pakadali pano, apolisi akusakasaka a Steve Kathala kuti akayankhe mulandu okupha munthu akapezeka olakwa mu bwalo la milandu.

Patrick anali wa m’mudzi mwa Mpholiwa mdera la mfumu yaikulu Njema ku Mulanje.

 

 

You May Also Like

ZIMENE MUMAKONDA

Please enter your comment!
Please enter your name here

From The World