Bungwe lowona zakayendedwe ka madzi muchigawo cha ku mmwera la Blantyre waterboard ladula madzi ku nthambi ya za chipatala mu mzinda wa Blantyre chifukwa changongole yomwe nthambiyi ili nayo ku bungweli.

Wamkulu owona ntchito za chipatala mumzinda wa Blantyre a Gift Kawaladzira watsimikza zankhaniyi.

Mukuyankhula kwawo a Kawaladzira anati nthambiyi ili ndi ngongole zokwana 1.5 miliyoni kwacha ku bungwe lowona za madzili.

Iwo anati abweza ngongoleyi boma likapereka ndalama kuthumba lanthambi la zaumoyo mwezi uno
wa July.

“Tiyesetsa kubweza ngongoleyi boma likatipatsa ndalama mwezi uno, anthu asadere nkhawa,” Anatsimikiza a Kawaladzira.

Gate way ndimbali imodzi yomwe yakhudzidwa ndi vutoli.

Pakadali pano ofesi ya nthambi yazachipatala ya mu mzindawu ndiyomwe ikupereka madzi atsiku ndi tsiku mmalo onse okhudzidwa.

You May Also Like

ZIMENE MUMAKONDA

Please enter your comment!
Please enter your name here

From The World