Ogwira ntchito a police ya Dedza adandaula kamba kosowa ukhondo pa office yawo chifukwa chopanda chimbudzi.

Ena mwa a polisi okhudzidwa Avomereza zankhaniyi ponena kuti tsopano chaka Chatha alibe chimbuzi cha anthu ogwira ntchito ponena kuti chimbudzi chomwe chinalipo potsegulira polisiyi chinaonongeka.

Iwo anapitiliza kunena kuti chimbudzi chomwe chilipo ndi cha anthu oganiziridwa kuti alakwira malamulo ndipo ulamuliro wa pa ufosiyi sukuonetsa chidwi chofuna kuthana ndi vutoli.

Poyankhulapo pa nkhaniyi othandizira mneneri wa polisi pa ofesiyi a Cassim Manda anadzudzula ogwira ntchito pa pilisiyi kuti adzitsata njira zoyenera popereka madando awo osati kudzera kwa atolankhani.

You May Also Like

ZIMENE MUMAKONDA

Please enter your comment!
Please enter your name here

From The World