Wolemba: Grecium Gama

Anthu omwe akumwa mankhwala otalikisa moyo a Edzi boma la phalombe awapepha kuti azikayezesa matenda achiwindi kuti moyo uzikhala wamphamvu.

Pepholi laperekedwa ndi ndi mkulu woyang’anira matenda a Edzi boma la phalombe a Harlod Mwaleya pa mwambo omwe bungwe la Just Associates (JASS) limakhazikisa buku lomwe lakodza lokhuza matenda a edzi la HIV Literancy manual Treatment.

Malingana ndi a Mwaleya anthu omwe akumwa mankhwala aARV akuyenera kukayezesa matenda a chiwindi kaamba koti mankhwalawa amasokoneza kagwiridwe ntchito kachiwindi.

“Tikupepha kuti wina aliyense amene amamwa mankhwalawa azipita kuchipatala kukayezesa mnthendayi kaamba koti ndiyoopsya ngati sitinaitulukire mwasanga koma ndiyochizika”.Mwaleya adofotokoza.

Sibongire Chibwensengini ndi mkulu woyanganira ntchito za bungwe la JASS ndipo anapepha anthu abomalo kuti agwiritse bwino ntchito bukhu lo kuti umoyo wawo ukhale waphamvu.

“Bukhu limeneli liwathandiza anthu aboma lino maka omwe amagwira ntchito za umoyo komanso amene anapezeka ndi kachilombo koyambisa matenda a edzi ndipo akumwa mankhwala otalikisa moyo”.Chibwesengini akufotokoza.

Iye adapephanso anthu ogwira ntchito zachipatala ena dziko muno omwe samaladira kapena kumvera za mmene wodwala akudandaula kuti achepese mnchitidwewu.

Bungwe la JASS likugwira ntchito ndi azimayi omwe anabwera poyera kuti anapezeka ndi kachirombo ka Edzi boma la phalombe .

AUZENI ANZANU PA
Yapita ijaFake doctor sentenced to 54 years imprisonment
Robert Ngwira
Attended Our Future Private Secondary School in Rumphi from 2006-2009 Holder of Diploma in Journalism from Malawi Institute of Journalism (MIJ) Hobbies, reading newspapers, going out with friends, listening to radio and watching football.

You May Also Like

ZIMENE MUMAKONDA

Please enter your comment!
Please enter your name here

From The World