Patadutsa nthawi yayitali pakumveka mphekesera zoti chipani cha Democratic Progressive (DPP) chagula ndege pokonzekera kampeni yamasankho omwe achitike chaka chamawa, chipanichi kudzera mwa m’neneri wake bambo Nicholas Dausi chafika poyera tsopano kutsimikiza zankhaniyi.

Malingana ndi bambo Dausi, chipani chawo cha DPP tsopano chamaliza kuchita dongosolo lonse loti ndegezi zomwe ndi ziwiri zamtundu wa ‘helicoptor’ zibwere m’dziko muno.

Bambo Dausi ati, DPP inagula kale ndegezi ndipo chomwe chatsala ndichakuti zibwere m’dziko muno koma iwo akana kunena tsiku lenileni lomwe ndegezi zitere panthaka ya Malawi.

(Visited 7 times, 1 visits today)

0

Subscribe to our Youtube Channel :

Follow Us on Instagram