Phungu wa kunyumba yamalamulo woyimila Phalombe Central Felton Mulli yemwe ndi mphwawo wa munthu wa mkulu pa business Leston Mulli ( Muli brothers), watsutsa mphekesera zomwe anthu ena akufalitsa zoti anamuwona akutuluka ndi Benerdeta Mlaka Maliro yemwe ndi mkazi wa mnyamata uja woyimba nyimbo za uzimu Mlaka Maliro ku Afrol Motel yomwe ili pafupi ndi depot ya wenela ku Blantyre dzana lachiwiri pa 09/07/2013 around cham’ma 04:17pm.

Malingana ndi bambo Mulli, iwo anasiya kunyengana ndi Mkaziyu yemwenso ndi phungu wa Chikhwawa Central m’mwezi wa November chaka chatha atawona kuti kunyenga mkazi wamwini ndi kulakwa komanso tchimo pamaso pa Mulungu kotero ati mphekeserazi sizowona.

(Visited 97 times, 1 visits today)
Subscribe to our Youtube Channel :


Follow our Instagram