Callista succeeds in removing Mutharika’s children as managers of K61bn estate
Former first lady Callista Mutharika has so far succeeded in her pursuit to remove former president Bingu wa Mutharika’s daughters, Duwa and Tapiwa as administrators of the controversial deceased’s estate.

Mkazi wa malemu Prof. Bingu Wa Muthalika ‘Callista’ wati, iye tsopano ndiwokondwa kuti Duwa ndi Tapiwa omwe amayendetsa chuma cha Bingu achotsedwa pa udindowu potsatira dandawulo lomwe iye anapereka ku bwalo lamilandu la High Court masiku apitawo.

Callista wati, panalibe chanzeru kuti anawa adziyendetsa chumacho popanda iye kutengapo gawo ngati mkazi wamalemu Prof. Bingu wa Muthalika, ndipo apa tsopano ndiwosangalala kuti asankha anthu ogwirizira chabe omwe adziyendetsa chumachi m’malo mwa iye ndi ana amalemuwa.

Anthuwa ndi Lawyer Kalekeni Kaphale yemwe adzithandizana ndi Modecai Mshisha m’malo mwa ana a malemu Muthalika ndipo iye( Callista) adziyimilidwa ndi bambo James Tomoka.

(Visited 8 times, 1 visits today)
Subscribe to our Youtube Channel :


Follow our Instagram