A police ku Mzuzu akusungira m`chitokosi msing`anga wa zaka makumi awiri ndi zisanu pa mulandu ogona ndi msungwana wa zaka khumi ndi zitatu.

Msing`angayi ndi Charles Muwa yemwe amachokera m`mudzi mwa Kulola mfumu yaikulu Mkanda M`boma la Mulanje.

Wachiwiri kwa M`neneri wa apolisi ku Mzuzu, Cecilia Mfune wati msungwanayi anachoka ku Ekwendeni loweruka komwe amakhala ndi agogo ake kupita ku Chibavi kwa mayi ake.

Ali ku Chibavi, anapezeka wasowa kotero mayi ake anadziwitsa anthu ozungulira za nkhaniyi.

“Atafufuzidwa komwe ali, anapezeka kunyumba ya msing`angayi yemwe amakhalaso m`mudzi omwewo,” malingana ndi a Mfune.

Msungwanayu anaulura kuti anagona kunyumba kwa msing`angayi komweso anamuchita zadama.

Bambo Muwa akuyembekezeka kukaonekera ku bwalo la milandu komwe  akayankhe mulandu ogona ndi mwana wachichepere.

(Visited 12 times, 1 visits today)

0

Subscribe to our Youtube Channel :

Follow Us on Instagram