Dziko la Uganda latseka nyumba zoulutsira mawu zokwana 23 chifukwa cholimbikitsa mchitidwe wa ufiti.

ntchito zoulutsa mawu

Malingana ndi malipoti, nyumba zoulutsira mawuzi zakhala zikupereka mwayi kwa asing’anga osiyanasiyana kuzasatsa malonda awo komaso kuuza anthu kuti amachiza matenda ngati Edzi kudzera mu zisamba.

Kotero mauthenga ngati awa akhala akulimbikitsa anthu kukhulupilira zitsamba komaso mwa zina, anthu ambiri aberedwa ndalama ndi asing’anga powakhulupilira kuti atha kuachiza matenda osiyanasiyana monga Edzi.

Pakadali pano, boma lalanda misonkho mpaka nyumba zoulutsa mauzi zitagwirizana ndi kutsatira zomwe boma la Uganda likufuna pakagwiridwe kawo ka ntchito.

Dziko la Uganda lili ndi nyumba zoulutsira mawu zokwana 292 zomwe zambiri mwa izo ndi zoyendetsedwa ndi anthu osati boma.

(Visited 19 times, 1 visits today)
0

Subscribe to our Youtube Channel :

Follow Us on Instagram