Mzibambo wazaka makumi awiri ndi zitatu yemwe akuganiziridwa kuti ndi wodwala nthenda ya misala wakwidzingwidwa ndi apolisi atapezeka atavala unifolomu ya apolisi pa msewu.

Malingana ndi Mneneri wa apolisi ya Kanengo Laban Mkalani, mzibamboyu yemwe dzina lake ndi Alim Amin ananjatidwa m’mawa wa lachitatu pa 4 Malichi.

A Makalani ati Amini adamangwidwa ndi apolisi omwe amalondera pa tsikulo. Akuti Mzibamboyu anakwidzingidwa munsewu wa thala wa Chendawaka akuimitsa magalimoto ngati ndi wa polisi wa pa msewu.

Chodabwitsa chinali chokuti, ngakhale anatchena bwinobwino zovala za apolisi komaso chipewa, ku mapazi ake anali asanavale kalikonse.

Pakadali pano, munthuyu akusungidwa pa polisi ya Kanengo pamene apolisi akupanga kafukufuku oti adziwe ngatidi ali wamisala komaso komwe anatenga yunifolomu ya apolisi.

Amin amachokera mdera la Mfumu yaikulu Kabudula ku Lilongwe.

 

(Visited 4 times, 1 visits today)

0

Subscribe to our Youtube Channel :

Follow Us on Instagram