Doloto wachinyengo¬†Clifford Chimtengo anapeleka mankhwala osakhalabwino kwa anthu anayi m’mudzi wa Joshua m’boma la Ntchisi.

Elise Kapolo (kumam’zere) ndi amuna awo bambo Bizaliele.

Dotoloyo anawanamiza anthu am’mudziwo kuti iye ndi dotolo ndipo amagwira ntchito ku chipata cha Queens mum’zinda wa Blantyre.

kenako dotoloyu anapereka mankhwala kwa anthu anayi ndipo patapita ma ola angapo anthu anayiwa anadwala mwakayaka. Athuwa anawatengela ku chipatala cha Ntchisi chomwe chili kutali ndi mudziwo.

Izi zizanachitika pakati pa usiku ndipo atafika nawo anthuwa kuchipatala, Liviness Kapolo wazaka makumi asanu ndi atatu ndi chimodzi (81) anali atamwalira. Livinesi wasiya zidzukulo zisanu ndi zinayi zomwe amaziyang’ala.

Anthu atatu ena , Bizaliele Kapola mlongo wa Liviness ndi mkazi wa Bizaliele, Elise Kapolo ndi Yohane Chipokosa akupezako bwino ndipo akulandila mankwala pachipatalapo.

“Linali tsiku langa loyamba kuona munthuyo m’mudzi mwathu koma anthu ena amati adamuonapo ndipo m’kachiwiri kumuona”¬† Elise adafotokoza motero.

” Iye adatiuza kuti ndi dokotala am’kagwira ntchito ku Queens ndipo amakhala m’mudzi oyandikila ko Khuwi” Elise adaonjera mawu.

Pakadali Pano apolisi¬† anjata¬†Clifford Chimtengo, Dotolo wachinyengoyo ndipo ali muchitolokosi kudikila m’landu wakupha munthu.

(Visited 16 times, 1 visits today)
0

Subscribe to our Youtube Channel :

Follow Us on Instagram