Mzika yaku Ameriaka Ya zaka  47 yomwe imapanga bisinesi ya phedwa ku nyumba yake m’bola ala Nkahatabay lachisanu sabala latha pa 20 july, 2018.

Omwalirayu amatchedwa Michael James Maglioli ndipo kwawo ndiku Massachusetts ndipo adaphedwa ku nyumba yake  yomwe ili m’mbali mwa nyanja ya Malawi.

M’neneri wa polisi Cecilia Mfune wanena kuti Michael amagulitsa mowa komanso zakumwa zozizilitsa ku khosi M’bomali.

Mayi ogwira ntchito zapa khomo pa bamboyo adena kuti iwo adamva munthu akugogoda ndipo  chitseko chidatsekulidwa poganiza kuti adali anthu ozagula zakumwa.

Mayiwo adali odabwa powona munthu wachilendo atavala chigoba ndipo adanyamula chikwanje.

Mbavazo zinanjata Michael kenako adamupha monvetsa chisoni.

Kafukufuku kuuchokera ku chipatala waonetsa kuti mzika yaku Americayi idafa chifukwa idataya magazi ambiri kudzera m’mabala omwe adali m’mutu mwake.

(Visited 10 times, 1 visits today)

0

Subscribe to our Youtube Channel :

Follow Us on Instagram