Mkhalakale pa za malonda yemweso ali wa pa mpando wa Mulhako wa Alhomwe, Leston Mulli watsimikizira mtundu wa amalawi poyera kuti chipani cholamula chomwe mtsogoleri wake ndi Arthur Peter Mutharika ndi cha alomwe okha basi.

Mulli

Bambo Mulli ayankhula mawuwa mu sabata yangothayi pa msonkhano wina omwe anachititsa.

Malinga ndi a Mulli, chipani cha DPP chinayamba ndi malemu Bingu wa Mutharika omwe amachokera ku Thyolo komwe ndi dera limodzi lomwe alomwe amachokera  chimodzi modzi ndi ku Mulanje komanso Phalombe.

Chifukwa cha chimenechi, a Mulli awuuza alhomwe onse kuti nthawi zonse ayenera azikhala pambuyo pa chipani cha DPP kamba koti chinayambitsidwa ndi Mlhomwe mzawo.

“Ndi chipani cha a Mbuyathu a Bingu, wina aliyense asatipitise kwina,”anawuuza anthu omwe anali pa msonkhanowo.

Mawu a Mulli akudza panthawi imene mtsogoleri wa United Transformation Movement (UTM) Dr Saulos Chilima komanso anthu ena akudzudzula akuluakulu a DPP kamba ka mchitidwe wosankhana mitundu mu chipanichi.

Malipoti akuonesa kuti anthu omwe amapatsidwa maudindo aakulu akulu mu chipanichi amakhala ochokera kum’mwera komwe kuli anthu ambiri amtundu wa chilhomwe.

(Visited 5 times, 1 visits today)

0

Subscribe to our Youtube Channel :

Follow Us on Instagram