Ku Malawi kuli luso mtheradi, monga mukuona pa chithunzi chiri mmusimu, chikuonetsa pool table yomwe anakonza ndi ana achisodzera ku Monkey-Bay.

Tebuloyi ndi sampulo ya pool tabel yomwe ndiyodula kuigula kotero ana achicheperewa adaganiza zomanga tebuloyi kuti asamatayitse nthawi yawo pogwira ntchito za asodzi ku Monke-bay.

Tebuloyi ndiyomangidwa ndi njerwa, dothi, neti ndi mateyara okutha. Anawa adakonza tebuloyi potengera pool tabele yeni yeni.

M’modzi mwa anawa dzina lake Vinicent adaganiza zo konza chinthuchi ndipo payekha sakadakwanitsa kotero adauza amzake kuti akonze chinthuchi.

pakadali pano anawa amakhala mosangala kamba masewero amaseweredwa pa tebulo amabweretsa chisangalaro pakati pawo.

Ukadaulo oterewu umabweretsa msangulotso pa kati pa ana. Monga tebulori likuonekera mutha  kuona kuti likufanana ndi pool table ili pachithunzi m’munsi.

 

(Visited 45 times, 1 visits today)


Subscribe to our Youtube Channel :

Follow Us on Instagram