Apolisi ku Chikwawa anjata m’dalala wa zaka makumi awiri ndi zitatu kamba kokuba mwana wazakazitatu ndikumu jadula (m’dulidwe) popanda chilorezo cha makolo amwanayo.

Mneneri wa polisi, Constable Foster Benjamin, wanena kuti mkuluyi dzina lake ndi Symon Kayiya ndipo amazitcha Ngaliba potengera chikhalidwe chake.

“Kayiya ananyengerela mwanayi ndi ndalama kuti akamugulira filizesi ndipo adatengela mwanayu pa tchile pomwe adagwiritsa ntchito mphanvu pa mdulidwe wa mwanayu” Costable Benjamin adalongosola motero.

Ndipo mwanayu adafooka kwambiri kamba adakakamizidwa kuti amwe phala la moto.

Izi zidachititsa makolo a mwanayo kutsina khutu apolisi pa nkhaniyi. Ndipo Kayiya wanjatidwa ali muchitolokosi cha polisi ku  Chikwawa.

(Visited 4 times, 1 visits today)
0

Subscribe to our Youtube Channel :

Follow Us on Instagram