Mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika wanena kuti dziko lino la Malawi lilibe zinthu loziyenereza kunkhazikitsa ntchito za chitukuko zomwe anthu ena akulonjeza kuti adzapanga ngati angawasankhe kunkhala atsogoleri a dziko lino.

A Muthalika apereka chitsanzo cha mwayi wa ntchito kwa anthu 1 Miliyoni m’chaka chimodzi komanso kunkhazikitsa mawulendo asitima za makono zomwe wachiwiri wawo a Dr Saulos Chilima wankhala akulonjeza.

Ndipo a Peter Munthalika anena kuti m’dziko muno mulibe mphamvu za magetsi okwanira kuchitira zitukuko.

Iwo alankhula izi dzuro pa m’sonkhano womwe adachititsa ku Nkhotakota pa ulendo wawo wobwerera ku Lilongwe kuchokera ku Mzuzu.

(Visited 11 times, 1 visits today)

0

Subscribe to our Youtube Channel :

Follow Us on Instagram