Mtsogoleri wa chipani cha Malawi Congress Lazarus Chakwera wapempha ma bungwe ofufuza za milandu ya katangale kuti afufuze ndi kuzenga mlandu onse amene akukhudzidwa ndi K145 million yomwe chipani cholamula cha DPP chidubweza kwa Pioneer Investments.

Lipoti la bungwe lofufuza za katangale la ACB likusonyeza kuti chipani cha DPP chidalandira ndalamazo mwachinyengo kuchokera kwa Pioneer Investments mu chaka cha 2016 pamene kampaniyi imagwira ntchito yoperekera zakudya ku Malawi Police Service.

Poyankhulapo pa nkhani yobweza ndalamayi Chakwera wati nkhaniyi ifufuzidwe kotheratu ndipo onse okhudzidwa azengedwe mulandu.

(Visited 9 times, 1 visits today)
0
Subscribe to our Youtube Channel :