Nthambi ya boma ya za kafukufuku ya National Statistical Office (NSO) yati izatulutsa zotsatira zakalembera wa nyumba ndi anthu mwezi wa December chaka chino.

Poyankhula ndi olemba nkhani mumzinda wa Blantyre lolemba, komishonala wa za kafukufuku ku NSO mayi Mercy Kanyoka ati padakali pano ali mkati momalizitsa ntchitoyi.

Kalembera wa nyumba ndi anthu wa chaka chino anafika kumapeto pa 23 September.

(Visited 5 times, 1 visits today)
Subscribe to our Youtube Channel :


Follow our Instagram