Mkulu oyang’anira za chisankho ku chipani cholamula cha Democratic Progressive Party (DPP), a Ben Phiri auza anthu kuti mtsogoleri wadziko lino Peter Muntharika ndi Maliseche awo.

a Ben Phiri pa msonkhano

A Ben Phiri ayankhula mawuwa ku msonkhano wa chipani cholamulachi ku Zomba omwe cholinga chake unali kumema anthu kuti akalembetse mavoti kuti azasankhe a Peter Mutharika.

M’mau awo, a Phiri anayerekeza a Peter Mutharika ndi maliseche ponena kuti munthu umabisa maliseche ako choncho anthu aku Zomba akuyenera kukavotera a Peter Mutharika pa zisankho za 2019.

“Maliseche munthu umabisa ako. Ife wathu kum’mwera kuno ndo professor Peter Mutharika basi. Maliseche athu ndi amenewo,” anatero a Phiri.

Koma anthu ena adzudzula a Ben Phiri ponena kuti sadasakhe mawu abwino omuyerekezera mtsogoleri wa dziko linoyu.

Kanema yemwe akuonetsa a Phiri akukamba izi wafala pa tsamba la intaneti la facebook komanso whatsapp.

(Visited 18 times, 1 visits today)
0
Subscribe to our Youtube Channel :


Follow our Instagram