Apolisi anjata Mkulu wina wa zaka 23 ku Kasungu kamba kupha Gule wa mkulu (Chilombo), ndipo mkuluyi akudziwika ndi dzina loti McCloud Mtonga.

Mtonga adakumana ndi Guleyu  pa 11 December, 2018, ndipo Guleyu adayamba kuthamangitsa Mtonga motsatizana ndikukwapulidwa kwambiri.

Atatopa Mtonga analanda ndodo ya Guleyo, m’kuyamba kuchibwezera kwa Guleyo.

Mpaka Guleyo adagwa pansi, atapita naye Guleyo ku Chipatala,  madotolo analegeza kuti Guleyo wamwalira.

Gule wa Mkuluyi amadziwika ndi dzina loti Ganizani Soko ndipo izi zidachitika m’mudzi wa Chifisi, sub/TA Mnyanja ku Kasungu.

Pakadali pano McCloud Mtonga ali m’manja mwa apolisi.

(Visited 25 times, 1 visits today)


Subscribe to our Youtube Channel :

Follow Us on Instagram