Msungwana wa zaka khumi ndi zitatu (13) wazipha Kamba konenedwa ndi azinzake pa tsamba la intaneti lochezerapo la whatsapp.

Nkhaniyi yachitika mu dziko la South Africa ku Pretoria lolemba lapitali.

Malingana ndi malipoti, Msungwanayi wakhala akunenedwa ndi azinzake pa gulupu lina la whatsapp kwa sabata imodzi, zinthu zomwe zinachititsa kuti akwiye ndikuchotsa moyo wake.

eNCA yati mzake wa malemuwa yemwe amaphunzira naye pa sukulu ya Doorpoort mu dela la Gauteng anaopseza kuti atumiza chithuzi choonepsa maliseche a mtsikanayu pa gulupu ya whatsapp lomwe amachezerapo.

Izi zinachititsa mtsikanayu kudziwitsa aphunzitsi pasukulupo kuti achitepo kanthu.

Koma litafika lolembe, mayi amtsikanayu anadabwa atapeza mwana wawo atazipha cha ku m’mawa la tsikuli.

Nkhaniyi yadzidzimutsa anthu mdelari kotero apolisi ndi anthu am’maudindo apempha makolo kuti adzitha kuchitapo kanthu mwana wawo akadandaula pa nkhani iliyonse ingakhale yaing’ono.

 

(Visited 11 times, 1 visits today)

0

Subscribe to our Youtube Channel :

Follow Us on Instagram