Mbava zosadziwika bwino zathyola kachisi ya  Kansuswa Seveth-Day Adventist mudera la Mufulira ku Zambia ndipo mbavazo zaba zipangizo zogwilitsa ntchito popemphera ndi katundu wina okwana k2, 700.

Malingana ndi malipoti ochokera kwa akulu am’pingo awuza atolankhani kuti mbavazo zidathyola kachisilo pausiku walachiwiri, ndipo adapitiriza kunena kuti Mbavazo zathawa ndi katundu osiyanasiyana wa Tchalitchilo.

Munthu ongodutsa ndiyemwe odawona izi ndipo adathamangila kukawuza akulu ampingo omwe amakhala pafupi ndi kachisilo.

Akulu ampingo adakapereka lipoti kupolice ndipo apolisi  ali kalikiliki kusaka mbavazo

(Visited 21 times, 1 visits today)

0

Subscribe to our Youtube Channel :

Follow Us on Instagram