Mzibambo wina ku Rumphi akugwira ukaidi wa zaka 14 kamba koti mtsikana wina analota akugwililidwa ndi bamboyo.

Malingana ndi Martha Chizuma yemwe anakayendera ndende ya Rumphi lamulungu lathali, mkuluyo adamangidwa mtsikanayo atapereka umboni oti wagwiliridwa.

Pa khothi, mchemwali wa ogwiliridwayo adapereka umboni oti nayenso adamva mawu a mzibamboyo pa nthawi yomwe izi zinkachitika. Umboni wa anthu awiriwa udapangitsa kumupeza mzibamboyo olakwa pa mulandu ogwilira.

“Dzulo ndinakayendera ndende ya Rumphi komwe ndinamva mulandu wa munthu wina omwe unandikhuza kwambiri. Mzibambo wa ku Rumphi akugwira ukaidi wa zaka 14 kamba koti adagwilira. Mtsikana analota mzibamboyu akumugwilira ndiposo mchemwali wa ogwiliridwayo adapelekera umboni ponena kuti adamva mawu a mzibamboyu kotero adamangidwa, ” Chizumu dalemba pa tsamba la intaneti.

 

(Visited 6 times, 1 visits today)
0
Subscribe to our Youtube Channel :