
Mutharika asankha wankulu wa bungwe lazachisankho la MEC
Published on October 14, 2016 at 2:48 PM by Robert Ngwira
President Peter Mutharika wasankha Justice Jane Ansah kukhala wapampando wa bungwe lazachisankho la Malawi Electoral Commission (MEC).
Ansah walowa m’malo mwa malemu Maxon Mbendera omwe anamwalira mwezi watha atangogwa pa mpando ku Lilongwe akugwila nchito zina zokhuza ofesi yake.
Mlembi wamkulu wa boma a George Mkondiwa ati kusankhudwaku kukuyambila lero.
Justice Ansah anali judge ku bwalo la apilo.