Mneneri wa boma, a Nicholas Dausi apempha a Saulos Chilima kuti atule pansi udindo wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino.

Dausi

Malinga ndi a Dausi, a Chilima akhala akunena boma la DPP kuti ndi lakatangale komaso la tsankho, zinthu zomwe sizoyenera kuchokera pakamwa pa munthu yemwe ali m’boma momwemo.

A Dausi ati ndi zinthu zodabwitsa kuti a Chilima akukamba za katangele pano pamene zaka zinayi zapitazi pakamwa pawo panali potseka.

“Ngati kuli katangale, auzeni a Chilima atule pansi pa udindo wawo kuti akhale ndi kuyera mtima kwaoko. Mu ulamuliro wa demokalase, ngati mtsogoleri waona vuto ndi kayendetsedwe kena ka dziko amakhala ndi ufulu otula pansi udindo, “atero a Dausi.

Kwa nthawi yaitali tsopano, a Chilima akhala akunena poyera kuti mtsogoleri wa dziko lino olemekezeka Peter Muntharika akuyendetsa dzikoli mopanda chilungamo.

Iwo achenjezapo kuti atha kuyamba kuulura zina mwa katangale zomwe boma la DPP pansi pa utsogoleri wa a Muntharika lakhala likupanga.

Kaliati

Poikirapo ndemanga, a Patricia Kaliati omwe aliso mu Mgwirizano wa a Chilima otchedwa United Transformation Movement (UTM), ati a Chilima sangatule pansi udindo wawo mpaka pa tsiku lomwe amalawi azakhale akukaponya voti mu 2019.

Posachedwapa, a Chilima auza mtundu wa amalawi ku msonkhano omwe anachititsa ku Lilongwe kuti boma la DPP lagula chipangizo chomwe likufuna kugwiritsa ntchito pozabera zisankho zikubwerazi.

Koma mbali ya boma latsutsa za nkhaniyi.

You May Also Like

ZIMENE MUMAKONDA

Please enter your comment!
Please enter your name here

From The World