Malingana ndi kafukufuku omwe BNM yachita, achinyamata omwe asankhidwa kuti akagwire ntchito ku Korea, azikalandila pafupifupi K413,000.00 ya Malawi pamwezi. Komabe ngakhale izi zili choncho, nkhawa ndiyakuti sizinadziwikebe kuti kodi achinyamatawa azikagwira ntchito yanji polingalira ndi kuchuluka kwa ndalama zomwe azikalandilazi. Kodi mwina ndiyodyetsa ng’ombe? Kugawula m’minda?, Kutibula mphanje? Kusenza Matumba amanyowa?. Ndichifukwa chake anthu ena akunena kuti, ana amabwana omwe atengedwa pa ulendowu akuganizilidwa kuti atha kukathawako chifukwa cha ntchito yokaka yomwe ili kumeneko.

(Visited 4 times, 1 visits today)
Subscribe to our Youtube Channel :


Follow our Instagram