Takulandirani pano pa Poly
Mudziwe icho khwalala lotchedwa
Masauko Chipembere
Adaliyikira m’khundumu
mwathumu
Omanga msewuwa ankadziwa,
ophunzira apa Poly ndi ine dziko
Akadandaula osaveka zinthu,
azikatseka msewuwo zinthu
ziyende msanga
Takulandirani
Mwafika panomu
Ndinu anthu ofunika kwambiri
m’dziko la Malawi
Mudakapita ku Chanco, enanu
bwezi muli a phunzitsi a Tikwere
Kapena a sukulu zakwacha
Mumvekere, “aphunzitsi, auzeni
ana aloze Kalulu ndi Fisi pa
bolodi”
Apo bi, enanu bwezi
mukuphunzira Chichewa
Chichewa cheni cheni mpaka zaka
zinai
Ku sukulu ya ukachenjede
timaphunzira mchichewa?
Mudakapita ku Bunda
Mwafikamu, bwezitu aliyense
atamugaira khasu ndi khwangwa
Okaswa mphanje ku Dzalanyama
Enanu bwezi mukuthena ng’ombe
Apo bi,
tikucheza panomu, enanu bwezi
mukusakaniza manyowa
Munthu oganiza ndithu
Angapite ku koleji kukaphunzira
za manyowa mpaka zaka zisanu?
Ku Bundako,
M’malo molimbikitsa uchembele
wabwino wa anthu
Iwotu amalimbikitsa uchembere
wa ziweto
Mesa m’malimbikira sukulu
kukana kulima?
Ndichifukwa chake mwadza pano
Pathumbi la mitu yokungidwa ndi
nzeru zakuya
Mudziwe Poly ndiyo imanga
Malawi
Ku Medicine
Nkhope zachimwemwezi bwezi
zitatha
Masana usiku kuyeza mitembo
kokhakokha
Nkhope zokongolazi
Pano zitakumbika ndi misozi
Kusewera ndi zidole mpakana
dzuwa tswi
Mkalasi ku Mediciniko, Amakhala
anthu seven
Mphunzitsi akati pangani magulu
seven, aliyese amapanga gulu lake
Mudakakwanitsa inu?
Ku Medicinitu
Kulibe kuyambitsa nyimbo
mokweza
Nanga simaliro samatha
Ukatitu wafika pa Medicine
Umachita kudziwiratu
Uli pasiwa mpaka pamene
udzamalize maphunziro ako
Ku KCN
Anyamata, bwenzi muli ma mid
husbands
Nanha si atsikana amati ma mid
wives
Zimatikhudza, akatipeza azathu a
ma College akuthengeko
Kulephera kuwoloka nseu
Ena mpaka kulephera kutuluka
Mushoprite, akuti potulukira
sapaona
Koma mwafika panomu
Muphunzira ntchito zosunga
Malawi
Polytu si College, ndi University
Mudzavetsere amati
Chancellor College
Bunda College
Kamuzu College of Nursing
College of Medicine
Iyi ndi University of Malawi – The
Polytechnic
Chizindikiro kuti mitsuko
yodzadza ndi nzeru zakuya
Idachita sung’uza pathundu lino
Ku Chanco
Bwezi enanu nkhope zitatupa
Ndi kachasu wa midzi yaku
Chilunga
Panotu wokumwa mowa
Amamwa mowa wa anthu
ophunzira
Mwana wa pa Poly
Akamayenda ndi anzake
Apa Bunda, Chanco, KCN ndi COM
Amachita kuwonekera patali
Kuti uyo, wapa Poly
Mwafika panomu
Dziwani tikonda kusewera ndi a
Police
Ikakhwithima sukulu
Timapempha ngati apolice ali pa
mpata
Komanso ngati chimbaula chili
bwinobwino
Tithamangitsane ko kulimbitsa
thupi
Ku KCN
Kuli uniform
Ku university amavala uniform?
Paliponse pamene ayenda
Ndi mbe mbe mbe
Ku sukulu ya mkaka uniform
Ku primary uniform
Ku secondary uniform
Mpaka ku Universityso uniform?
Kwatsala ndiku pisila
Tidzangova ayamba kuwapisilitsa
ku KCNiko
Pano pa Poly
Timu ya mpira wamiyendo
Ma pulakatisitu imakachitira pa
Kamuzu Stadium
Pomwe azathuwa amangoimva
pa wailesi
Mchifukwa chaketu tsono
Kholo lizindikira likamalangiza
mwana limati
“Mwana wanga paja umafuna
kukaphunzira kuti?”
Mwana akati “ku Chanco”
Limamuwuza “Kazisewera mwa
ufulu”
Opita ku Poly, nthawi yosewera
alibe.

(Visited 6 times, 1 visits today)
Subscribe to our Youtube Channel :


Follow our Instagram