Nduna yadzachilungamo mdziko muno ‘Ralph Kasambara’ yachenjeza wachiwiri kwa President wadziko lino bambo Khumb Kachali kuti amugulura mano akapitiliza zomamukhomelera.

Chidani cha mamulumuzanawa, chidayamba kuchokera pomwe Kachali adakaniza Kasambara contract yonyamula fetereza wa ‘Subsidy’ ndipo kuti m’malo mwake, adangophangira yekha.

Kuchokera apa, makosanawa sayang’anizana diso la bwino ndipo mphekesera yomwe yatipeza ndiyakuti Kasambara wachenjeza mkuluyu kuti amutidzimula ngati, angapitilize kumamukhomelera kwa JB chifukwa zamukwana.

(Visited 9 times, 1 visits today)
Subscribe to our Youtube Channel :


Follow our Instagram