Akuluakulu a chipani cholamula boma cha PP ati, sakupenekera konse kuti moto womwe watentha ma hostel anyamata pa sukulu ya Joyce Banda Foundation yaku Chimwankhunda ku Blantyre, anayatsa ndi a chipani cha DPP.

”ife sitikupenekera konse kapena kuchotsera kuti anachita zawupanduzi ndi achipani cha DPP chifukwa sakugona tulo ndi Mayi Joyce Banda. Akufunafuna njira zoti awagonjetse koma akulephera ndinkuwona achita izi. Koma ndiiiiiithu, anjatidwa posakhalitsa pamodzi ndi amene akuwatumayo” ayankhula chonchi mamulumuzanawa.

(Visited 26 times, 1 visits today)


Subscribe to our Youtube Channel :

Follow Us on Instagram