Potsatira kufala kwa mbozi zatsopano zotchedwa Ntchembere zandonda zomwe zikusowetsa mtendere poteketa mbewu m`minda yambiri, alimi tsopano ayamba kugwiritsa ntchito njira zina za makolo poyesayesa kuthana ndi mbozizi.

chitsanzo cha mbewu zoteketedwa ndi ntchembere zandonda

Malingana ndi wachiwiri wa sikimu ya nthilira ya Kambwiri Sele ku Salima, Batimeyo Malenga, madzi otsukira usipa owuma ophatikiza ndi shuga komanso madzi a tsabola ndi njira zamakolo zomwe alimi ambiri ayamba kugwiritsa ntchito sopano.

alimi tsopano ayamba kugwiritsa ntchito njira za makolo pothana ndi mbozi zonga izi

Monga madzi otsukira usipa owuma ophatikiza shuga akathiridwa pa mbwewu amakopa nyerere zomwe zimabwera pa mbewuzo zomwe zotsatira zake zimadya mbozi zomwe zimadza ndi cholinga chozateketa mbewuzo.

“Timagwiritsa ntchito malita asanu a madzi potsuka usipa, kenako timathira shuga m`madziwo omwe timawawaza m`minda mwathu.

“Fungo la usipa komanso kukoma kwa shuga kumaitana nyerere zomwe zimabwera ndikudya mbozizo,” malinga ndi a Malenga.

Koma ngakhale izi zili chomwechi, mulangizi wa za ulimi m`boma la Salima, Martin Nuka wapempha alimi kuti azigwira ntchito limodzi ndi alangizi a zaulimi asanayese njira zina zatsopano.

Kuonjezera apo, boma la Malawi linapempha alimi kuti apewe mchitidwe ofuna kuyesa kuthana ndi mbozizi pogwiritsa ntchito njira zomwe iwo pawokha akuziona ngati zitha kuthandiza.

Boma linalimbikitsabe alimi mdziko muno kuti azigwiritsa mankhwala omwe ali ovomerezeka pofuna kuthana ndi mbozizi monga cypermethrine.

(Visited 14 times, 1 visits today)

0

Subscribe to our Youtube Channel :

Follow Us on Instagram