Njira Zitatu Zomwe ESCOM ingathetsere Vuto la kuthimathima kwa Magetsi

M`modzi mwa atolankhani a M`dziko lino yemwe amakhala ku souh africa, Harry Mangulenje wati ndi okhuzika ndi vuto la kuthimathima kwa magesi kotero wapereka njira zina zomwe ESCOM ingasate kuti vutoli lithe.

Umu ndimomwe walembela pa Facebook penji yake lero:

“Palibe chinthu chonyasa ngati kuthima kwamagetsi. Magetsi amene tikugwiritsa ntchito anakhazikitsidwa kale kwambiri.

Zulo talephela kugula laptop chifukwa kunalibe magetsi kuti tikanatha kuyesa.

Pano zinthu zayipa, mabusiness ndi ma factory akuyima chifukwa chakuthima kwamagetsi.

Ngakhale anthu ofuna kukhazikitsa ma company kuti adzilemba anzawo ntchito akulephela popeza magetsi kulibe.

Koma kodi vuto limeneli lingathe bwanji?

Nanga tsogolo lamagetsi ku Malawi lidzakhala lotani. Nanga tsogolo la ma business odalira magetsi.

Poyamba bungwe lamagetsi ndi boma asiye kumasokosa anthu ndi nkhani zoti akufuna kuwonjezela mphamvu mwakuti mwakuti.

Nkhani izi takhala tikudzimva kuyambila mma 1999 mpaka nthawi imene ku Escom kunali Padambo nyimbo yake inali yomweyo, kuti akufuna kuwonjezela mphamvu zamagetsi motere motere.

Ndi zinthu zauchisiru.

Ngati boma lili serious, lingowonjezela mphamvuyo mwakachetechete anthu awone kusintha.

Koma kodi njira zina zothetsera vutoli kupatula Solar zingakhale ziti?

Njira zothetsera vuto lamagetsi ziyenela kukhala mmagawo awiri. Long term and short term.

Kuchepetsa vutoli, lero komanso mtsogolomu.

Ine ndimakhulupilira kuti kuthimathima kwamagetsi sikumachitika chifukwa chakuchepa kwa mphamvu yamagetsi kokha.

Komanso chisokonezo pa kagwiritsidwe ntchito kapena mfundo zoyendesera kagawidwe kamagetsi.

Mwa ichi pamene boma linali likufufuza ndalama zogulira zipangizo zokudzira mphamvu zamagetsi linayenela kuthetsa chisokonezo pakagawidwe ndi kagwiritsidwe ntchito kamagetsi kuti lithe kuchipetsa kuthima thima kwamagetsi mwamsanga.

PREPAID SYSTEM

Mwachisanzo. Boma lilimbikitse mfundo za Prepaid.

Aliyense nyumba iliyonse iyenela kukhala Prepaid.

Komanso pogula magetsi anthu adzilowetsa Meter number yawo. Kusonyeza izilowetsa magetsi potsatira meter number.

Kotero kuti ngati nyumbayo ili ndivuto magetsi asamalowe mpaka vutolo litakonzedwa.

THRESHOLD

Pakuyenela kukhala malire akagwiritsidwe kamagetsi, kuti magetsi adzitha kukwanila dziko lonse.

Njira ya Threshold ndi imene ikugwiritsidwa ntchito ku South Africa ndipo ikuthandiza kwambiri maka mnyumba zawanthu.

Zimakhala chonchi. Pa mwezi uliwonse pamakhala malire pa nyumba iliyonse, kapena factory iliyonse pamagetsi omwe angagule pamtengo woyenela (wotchipa).

Ngati nyumbayo kapena factory idutsa malirewo imagula magetsi pa mtengo wokwera.

Mwachitsanzo tinene kuti Escom ikugulitsa magetsi pa MK10 per Unit.

Ndiye kuti nyumba iliyonse itha kugula magetsiu malire 1000 units pa mtengo wa K10.

Koma ngati nyumbayi ipitilira apo, mwezi usanathe, ndiye kuti magetsi owonjezelawo idzagula pa MK18 pa unit imodzi.

Chimodzi modzinso mma factory. Atha kuyika Threshold yoyenela mma factory. Zitha kuteronso ndimma gulu ena monga muzigayo.

Iyi ndi njira yabwino kusiyana ndikungokweza magetsi kwa aliyense.

Pamene anthu adzathe kumagwiritsa ntchito magetsi mosamala, magetsi adzatha kudzakwanila aliyense.

Tiyenela kudziwa kuti magetsi amathima maka chifukwa machine saakutha kupereka magetsi kwa anthu amene akufuna magetsi nthawi imeneyo.

Magetsi amayaka gulu la wanthu ofuna magetsi likachepa.

Ndizomvetsa chisoni kuti Esco imagaza kuti itha kuthetsa vuto lamagetsi pomangokweza mtengo kokha.

Escom ili ndi udindo wowonetsetsa kuti magetsi akugawidwa motsata ndondomeko ndi ukhondo wamagetsi. Pali nyumba ndi malo ena osayenela kukhala magetsi. Koma mudzapeza kuti kuli magetsi.

Izi ndi zina zomwe zimapangitsa ma black out.

Escom inayenela kulemba anthu ambiri ntchito kuti akhale oyendela (ma inspector) mmalo mmene magetsi akugwiritsidwa ntchito modetsa nkhawa kuti adzitha kudziwa zowona.

Pali anthu ambiri amene akugwiritsa ntchito magetsi mwaulele pogwiritsa ntchito njira zachidule zautchisi. Ena anapambutsa magetsi pansi pa nthaka popanda kutsata ndondomeko za Escom. Izi zimapangitsa kuti Machine adziona ngati anthu ogwiritsa ntchito magetsi ndi ochuluka kwambiri. Zotsatira zake ndi kuthimathima kopanda ndondomeko.

DEMARCATIONS OF LOCALITY

Escom itha kuchepetsa vuto lakuthima kwamagetsi pogawa mmadela mokhala anthu.

Mwachitsanzo,sipangakhale mulandu kusiyanitsa mmadela mokhala anthu ndi madela amafactory olo mmadela mokhala anthu OLEMELA ndi OSAUKA.

Mmadela mwa anthu olemela magetsi atha kukhala okwelerako mtengo kuposa mmadela awanthu wamba.

Kusiyana kwake kutha kukhala koti mmadela mokhala wanthu olemela magetsi atha kukhala osathimathima ngati mmadela mwa wanthu osauka.

Izi zitha kuchitika chifukwa cha mfundo za nyuwani zofuna kukonza vuto la kuthimathimaku.

Chonchonso mmadela mmene muli ma factory mutha kusiyanitsidwa ndi mmadela mmene mmangokhala wanthu chabe.

Kotero kuti mma factory magetsi sangamathimitsidwe ngakhala magetsi atathima mmadela mokhala wanthu.

Kukwanitsa ma plan ngati awa sikophweka kungafune ma expert odziwa kujambula maplan monga ma consultant. Koma ndizotheka ndipo Escom itha kuchepetsa phuma pankhani yamagetsi kwa zaka zochuluka kupita mtsogolo.”

0

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *