Polisi ya kanengo ku Lilongwe ikusungira mchitokosi mzim`bambo wa zaka makumi awiri ndi zitatu (23) pa mlandu wokupha mzim`bambo nzake wa zaka makumi atatu ndi zisanu (35) kamba ka mkazi.
Wachiwiri kwa ofalitsa nkhani pa polisi ya kanengo, Esther Mkwanda wati mzim`bamboyu yemwe dzina lake ndi Gift Sitina anabaya a Austin Chirombo lachinayi lapitali m`mudzi mwa Mchezi mdera la mfumu yaikulu Chimutu ku Lilongwe.
Malinga ndi a Mkwanda, Sitina anali pa banja ndi Mkazi wa malemuwa koma kamba ka nkhani zina banjalo linatha.
Ngakhale a Sitina akhala akuchondelera Mzimayiyo kuti abwelerane, palibe cha phindu chilichonse chomwe kuchondelera kwao kunaphula.
“Mosapanganika, zinachitika kuti a Sitina anayandikana ndi nyumba yomwe mkazi wawo wakaleyo amakhala ndi mwamuna watsopanoyo, malemu Chirombo. Chikondi cha anthu awiriwa chinafika pokoma mpaka a bambo Sitina anayamba kupanga nsanje,” anafotokoza a Mkwanda.
Pa tsikulo, bambo Sitina adapita kunyumba kwa a Chirombo atanyamula mpeni m`manja omwe anagwiritsa ntchito pobayira bambo mzawoyo.
Mwatsoka a Chirombo anamwalira akufika ku chipatala cha Daeyang Luke. Zotsatira za ku chipatala zidaonetsa kuti malemu Chirombo adamwalira kamba kotaya magazi ambiri.
A Sitina amachokera m`mudzi mwa Dzuwa Mdera la mfumu yaikulu Mchiramwera ku Lilongwe ndipo akuyembekezeka kukaonekera ku bwalo la milandu komwe akayankhe mlandu okupha munthu omwe umatsutsana ndi gawo 209 la dziko lino.