Mkango olusa wavulaza anthu atatu m’boma la Chitipa pomwe amafuna kupha mkangowo.

Izi zachitika m’mudzi wa Kasisi pomwe anthu atatuwa amafuna kupha m’kangowu ndi mikondo komanso mkhwangwa, koma m’kanguwo unakwanitsa kuluma anthuwa kenako m’kuthawa.

Anthu ovulalawa akudziwika ndi maina awa Mabacha Sibale, Kauka komanso Haonga omwe amakhala m’mudzi momwemo.

Lion-Malawi

Mkango wavulaza anthu atatu

Anthu atatuwa awatengela ku chipatala Cha Kameme zinthuzi zitango chitika.

Pakadali pano apolisi anenakuti m’kangowu udakali kuyenda mu dera la Kasisi ndipo apeleka chenjezo kwa anthu am’derali kuti ankhale mosamala chifukwa cha mkangowu.

M’mawa wa lachinayi, Mneneli wa Polisi ku chitipa Gladwell Simwaka adanena kuti m’kangowo wakhala ukuvutitsa m’madera amfumu yaikulu Kameme T/A Mwaulambia m’boma la Chitipa.

Ndipo adaonjezera ponena kuti mkangowu akuwukaikira kuti wathawa ku malo osunga zinyama ku Luangwa mdziko la Zambia.

Mkangowu  wapha Ng’ombe zisanu ndi imodzi m’mudzi mwa Kasisi.

Pakadali pano apolisi ndi anthu oyang’anila zinyama akusaka saka mkangowu. Simwaka watero.

(Visited 13 times, 1 visits today)

0

Subscribe to our Youtube Channel :

Follow Us on Instagram