Scandal, Blantyre Kanjedza.

Mzimai wina ogwira ntchito ku NBS bank Mrs (Dzina la bisidwa) wagwidwa ali ndi chibwenzi chanseri, iwowa anali ndi chibwenzi mugalimoto yachibwenziyo panja munseu.

Ndiye amuna ake akubwera kuchokera ku ntchito anamuona mkazi wawoyo ali ndi njonda m’galimoto.

Njondayo itaona kuti zathina inayamba kuthawa ndi galimo ndipo mwini mkaziyo anayamba kuthamangitsa njondayo ndigalimoto yake pa mbuyo.

Patangotha kamtunda pang’ono galimoto ya chibwenziyo inakanika kuyenda bwino  ndipo anakanika kukhota mkukaomba mpanda wakwa neba mpaka kugwetsa Chipupa cha nyumba mkukaima ndi mtengo pamalopo.

Njondayo inathawa  wapansi m’kusiya chibwenzicho chili m’galimoto.

Mzimaiyo wavulala ndipo amuna ake atafika pamalopo  anamutenga.

Galimoto yomwe imagwiritsidwa ntchito ndi njondayo ndiyobwelekedwa.

Eniake anyumba yomwe ya gundidwa anena  kuti Njondayo yo idzaitenge galimotoyo kuti akambilane zomanga chipupa chanyumbayo njondayo yagunda ndi galimoto ili pa chinthunziyi.

Pakadali pano tili mkati mofufuza kuti m’zimai wa chisembwereyu zimuthera bwanji ndi mwamuna yemwe ali naye pa banja.

Nkhaniyi ya khala ikukambidwa kuyambira dzulo pa tsamba la facebook ndi WhatsApp.

(Visited 60 times, 1 visits today)
0
Subscribe to our Youtube Channel :


Follow Us on Instagram