Apolisi mtowinshipi ya Limbe ku Blantyre anjata kathyali wina kamba kukoba katundu okwana ndalama k2.2 million ndipo mkuyuyu dzina lake ndi Blessings Mtitule.

M’neneri wa polisi wa ku Limbe  Widson Nhlane wanena kuti analandila uthenga ku Chokera kwa anthu okhala ku Chinyonga pa 18 July, 2018 kuti mbava zathyola nyumba ya Mai wina ndipo zinaba makina akomputa, iphone, masipika komaso nsapato zachizibambo zokwana 12 ndi zovala zokwana k2,240,000.

Apolisi atapanga chipikisheni pa 23, Mtitule ananjatidwa ndipo anamupeza ndi katundu yemwe wa tchulidwayi.

Mneneri wa polisiyu wanena kuti adakali kalikiliki kufufuza kandundu otsala yemwe adabebwayo.

Pakadali pano apolisi amema anthu amderali kuti asanyozere kutsina khutu apolisi pankhani ya zimbalangondozi akaziona.

Mtitule amakhala m’mudzi mwa Mtalala, mfumu yaikule Nsomba ku Blantyre ndipo akuyembekera kukalowa Court sabata la mawa.

(Visited 9 times, 1 visits today)
0
Subscribe to our Youtube Channel :


Follow Us on Instagram