Mphenzi yaomba nyumba ndipo yapha mwana wa za zisanu ndi chimodzi wa m’mudzi mwa a Jalasi m’boma la Mangochi ndipo mphenziyi yapweteka nyamata wa zaka khumi ndi ziwiri wa m’mudzi momwemo.

Ngoziyi yachitika pa 27 November, 2018 m’munthawi ya 5 koloko madzulo m’mudzi mwa Balakasi.

Shanila Saidi wazaka makumi atatu ndi zisanu, yemwe ali mayi wa anawa adawuza apolisi panthawiyo kuti kunali mvula yambiri yomwe imagwa mophatikiza ziphaliwali (Mphenzi) ndipo izi zidachititsa anawa kuti kuti akause m’nyumba.

“Izi zidachitika pomwe mwanayo amakodza kudzera pa zenera la nyumbayo ndipo mphenzi idaomba ndikupha mwanayo pa malo omwewo ndi ku vulaza mwana m’modzi.” Mayi Saidi adatero.

 

 

(Visited 17 times, 1 visits today)

0

Subscribe to our Youtube Channel :

Follow Us on Instagram