Apolisi mu m’zinda wa Blantyre amanga nyamata wa zaka 22 kamba adamenya bambo ake mpaka kuwapha pa nkhani ya Mango.

Potsimikizira nkhaniyi, M’neneri wa Polisi Sub Inspector Augustus Nkhwazi yemwe wanena kuti nyamatayi dzina lake ndi Arthur Maliro ndipo wapha bambo ake odziwika ndi dzina loti George Maliro ndipo adali ndi zaka 58.

Malingana ndi Nkhwazi, Pa 16 December, 2018 pa nthawi ya 11am, Arthur Maliro amathyola mango pafupi ndi nyumba ndipo bambo ake adauza Arthur kuti asiye kuthyola mangowo kamba kokuti mangowo sadaphye.

Ndipo izi zidakwiyitsa Arthur, kenako adatola botolo la galasi ndikuwagenda bambo ake m’mutu.

Bambo Maliro adakomoka pomwepo ndipo adathamangila nawo ku chipala cha Mpemba komwe madotolo adanena kuti bambo Maliro amwalira.

Bambo George Maliro amachokera m’mudzi mwa Nsomba T/A Nsomba mu mzinda wa Blantyre.

Sub Inspector Nkhwazi, wanena kuti Arthur Maliro atengeledwa ku Court pomwe apolisi ali kalikiliki kufufuza za nkhaniyi.

 

(Visited 19 times, 1 visits today)


Subscribe to our Youtube Channel :

Follow Us on Instagram