Bungwe la anthu omwe amadwala matenda a Shuga lati kuchepa kwa zipangizo zofalitsira mauthenga a nthendayi m’madera akumidzi ndi chimodzi mwa zinthu zomwe zikubwenzeretsa mmbuyo ntchito yolimbana ndi nthendayi.

Mtsogoleri wa Bungweli, a Clement Mandala anena izi pomwe dziko la Malawi pamodzi ndi mayiko onse padziko lapansi akukumbukira tsiku loganizira za matenda a Shuga pa 14 November chaka chilichonse.

A Mandala anati ndizomvetsa chisoni kuti anthu ambiri akudwala komanso kumwalira ndi matendawa kaamba kosowa upangiri wa momwe angapewere nthendayi.

Source : Yoneco Fm

You May Also Like

ZIMENE MUMAKONDA

Please enter your comment!
Please enter your name here

From The World