Mzibambo wina M’boma la nsanje watsamira dzanja atamwa mowa kwambiri osadyera chakudya.

Apolisi ku Nsanje atsimikiza za nkhaniyi ndipo ati malemuwa ndi a Khembo Yobe azaka makumi anayi (40)

Malinga ndi wachibale wa malemuwa a Spear Khembo, malemuwa adachoka lolemba pa 12 Malichi ndi cholinga chakuti akaonere mpira koma ali komweko anapitilira ku malao omwera mowa komwe adayamba kumwa zakumwa zoledzeretsa ndipo sadabwerereso kunyumba pa tsikulo.

Usiku wa Tsiku lotsatira pa 13 Malichi, thupi la malemu Yobe lidapezeka munsewu m’mudzi wa Chiphwembwe M’boma lomwelo.

Azantchito za chipatala pamodzi ndi apolisi adapita pa malowo ndipo zotsatira za ku chipatala zidatsimikiza kuti a Yobe adamwalira kamba kokumwa mowa osadyera.

Malingana ndi malipoti, malemuwa akuti amadziwika ndi nkhalidwe okumwa mowa mwa uchidakwa.

A Yobe amachokera m’mudzi mwa Chiphwembwe Mdera la mfumu yaikulu Malemia ku Nsanje.

 

(Visited 6 times, 1 visits today)
0
Subscribe to our Youtube Channel :


Follow Us on Instagram