Apolisi m’boma la Mangochi anjata njonda ina ya zaka 31 zakubadwa a Henry Bauleni kamba kombela anthu m’boma la Mangochi.

Henry Bauleni

Tsizinamtoleyu wakhala akubera anthu kudzera pa Artel money kuchokera ku mayambirilo achaka chino ndipo anthu ambiri akhala akudandaula kamba koberedwa kudzera pa airtel money.

Pa usiku wa pa 23 july, 2018 apolisi aku Mangochi adakwanitsa kugwira bambo Henry kunyumba kwao m’mudzi mwa Mponda m’boma la Mangochi. Iwo adawanjata kamba apolisi akhala akufufuza  m’mene Njondayi imayimbira phone kwa anthu owabera.

Kafukufuku wankhaniyi akusonyeza kuti Njondayi idakwanitsa kuba ndalama zopyola k900,000 kwa anthu osiyana siyana kudzera m’ma agent a airtel money komanso amachotsa ndalama za anthu omwe ndalama zawo zili ku airtel money yawo.

Pafupifupi anthu makumi atatu adabeledwa ndalama ndi m’kuluyi powamema kuti apata mphoto kuchokera ku Airtel komaso amanamizira ngati kasitomara wotenga ndalama pa agent.

Apolisi atapanga chipikisheni nyumba ya njondayi anapezamo ma phone awiri komanso masimcard ankhaninkhani ndiponso adapeza kabuku komwe mudali manambala osiyanasiyana ndima nambala achinsinsi ake omwe amagwiritsidwa ntchito pobera anthu.

Mthambi ya Airtel ku Mangochi yatsimikiza zankhaniyi ndipo manambala anali mukabukulo angwirizanadi ndi manabala achinsinsi omwe anali mukabukuko.

Wankulu woyang’anira Airtel ku Mangochi wa chenjeza anthu kuti asamapereke nambala zawo za chinsinsi kwa anthu osawadziwa komaso azikhala ochenjera akaimbilidwa phone ndi anthu achilendo omwe akumakamba zakhudza mipikisano yosadziwika bwino pa phoni.

(Visited 8 times, 1 visits today)

0

Subscribe to our Youtube Channel :

Follow Us on Instagram